Daniel 6:7 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akulu onse a ufumuwo, ndi akazembe ndi akalonga, mandoda, ndi ziwanga, anapangana kukhazika lemba lachifumu, ndi kuikapo choletsa cholimba, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nduna zoyendetsa ufumu wanu, aphungu, akalonga ndi abwanamkubwa tonse tagwirizana kuti inu mfumu mukhazikitse lamulo ndi kulisindikiza kuti aliyense amene apemphera kwa mulungu wina kapena kwa munthu kupatula kwa inu mfumu, pa masiku makumi atatu otsatirawa, adzaponyedwa mʼdzenje la mikango.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akuru onse a ufumuwo, ndi akazembe ndi akalonga, mandoda, ndi ziwanga, anapangana kukhazika lemba lacifumu, ndi kuikapo coletsa colimba, kuti ali yense akapempha kanthu kwa mulungu ali yense, kapena kwa munthu ali yense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango,