Daniel 7:1 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chaka choyamba cha Belisazara mfumu ya ku Babiloni Daniele anaona loto, naona masomphenya a m'mtima mwake pakama pake; ndipo analemba lotolo, nalifotokozera, mwachidule.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chaka choyamba cha ufumu wa Belisazara wa ku Babuloni, Danieli akugona pa bedi lake analota maloto ndipo anaona masomphenya. Iye analemba malotowo mwachidule.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Caka coyamba ca Belisazara mfumu ya ku Babulo Danieli anaona loto, naona masomphenya a m'mtima mwace pakama pace; ndipo analemba lotolo, nalifotokozera, mwacidule.