Daniel 7:20 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi za nyanga khumi zinali pamutu pake, ndi nyanga ina idaphukayi, imene zidagwa zitatu patsogolo pake; nyangayo idali ndi maso ndi pakamwa pakunena zazikulu, imene maonekedwe ake anaposa zinzake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinafunanso kudziwa za nyanga khumi za pa mutu pake ndiponso ina ija, nyanga imene inaphuka pambuyo pake ndi kugwetsa zitatu zija. Imeneyi ndi nyanga ija yokhala ndi maso ndi pakamwa poyankhula modzitamandira, ndipo inkaoneka yayikulu kupambana zina zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi za nyanga khumi zinali pamutu pace, ndi nyanga yina Idaphukayi, imene zidagwa zitatu patsogolo pace; nyangayo idali ndi maso ndi pakamwa pakunena zazikuru, imene maonekedwe ace anaposa zinzace.