Daniel 7:25 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nidzanena mau akutsutsana ndi Wam'mwambamwamba, nidzalemetsa opatulika a Wam'mwambamwamba, nidzayesa kusintha nthawizo ndi chilamulo; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lake mpaka nthawi imodzi, ndi nthawi zina, ndi nthawi yanusu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Idzayankhula motsutsana ndi Wammwambamwamba ndipo adzazunza oyera mtima ndi kusintha masiku azikondwerero ndi malamulo. Oyera mtimawo adzalamulidwa ndi mfumuyi kwa zaka zitatu ndi theka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nidzanena mau akutsutsana ndi Wam'mwambainwamba, nidzalemetsa opatulika a Wam'mwambamwamba, nidzayesa kusintha nthawizo ndi cilamulo; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lace mpaka nthawi imodzi, ndi nthawi zina, ndi nthawi yanusu.