Daniel 7:4 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Choyamba chinanga mkango, chinali nao mapiko a chiombankhanga, ndinapenyera mpaka nthenga zake zinathothoka, nichinakwezeka kudziko, ndi kuimitsidwa ndi mapazi awiri ngati munthu, nichinapatsidwa mtima wa munthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Choyamba chinali ngati mkango, ndipo chinali ndi mapiko ngati a chiwombankhanga. Ndinayangʼanitsitsa, kenaka mapiko ake anakhadzuka ndipo chinanyamulidwa ndi kuyimirira ndi miyendo yake iwiri ngati munthu, ndipo anachipatsa mtima wa munthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Coyamba cinanga mkango, cinali nao mapiko a ciombankhanga, ndinapenyera mpaka nthenga zace zinathothoka, nicinakwezeka kudziko, ndi kuimitsidwa ndi mapazi awiri ngati munthu, nicinapatsidwa mtima wa munthu.