Daniel 7:5 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo taonani, chilombo china chachiwiri chikunga chimbalangondo chinatundumuka mbali imodzi; ndi m'kamwa mwake munali nthiti zitatu pakati pa mano ake; ndipo anatero nacho, Nyamuka, lusira nyama zambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo ndinaona chirombo chachiwiri, chimene chimaoneka ngati chimbalangondo. Chinali chonyamuka mbali imodzi, ndipo chinapana nthiti zitatu mʼkamwa mwake pakati pa mano ake. Anachilamula kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo taonani, cirombo cina caciwiri cikunga cimbalangondo cinatundumuka mbali imodzi; ndi m'kamwa mwace munali nthiti zitatu pakati pa mano ace; ndipo anatero naco, Nyamuka, lusira nyama zambiri.