Daniel 7:6 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pambuyo pake ndinapenya ndi kuona china ngati nyalugwe, chinali nao mapiko anai a nkhuku pamsana pake, chilombocho chinali nayonso mitu inai, nichinapatsidwa ulamuliro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pambuyo pake, ndinaona chirombo china, chimene chinkaoneka ngati kambuku. Pa msana pake chinali ndi mapiko anayi onga a mbalame. Chirombo ichi chinali ndi mitu inayi, ndipo chinapatsidwa mphamvu kuti chilamulire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pambuyo pace ndinapenya ndi kuona cina ngati nyalugwe, cinali nao mapiko anai a nkhuku pamsana pace, ciromboco cinali nayonso mitu inai, nicinapatsidwa ulamuliro.