Daniel 7:8 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinali kulingilirira za nyangazi, taonani, pakati pa izo panaphuka nyanga ina, ndiyo yaing'ono; patsogolo pake zitatu za nyanga zoyambazi zinazulidwa ndi mizu yomwe; ndipo taonani, m'nyanga m'menemo munali maso ngati maso a munthu, ndi pakamwa palikunena zazikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndikulingalira za nyangazo, ndinaona nyanga ina, yocheperapo, imene inkatuluka pakati pa zinzake. Zitatu mwa nyanga zoyamba zija zinazulidwa mwa icho. Nyanga iyi inali ndi maso a munthu ndi pakamwa pamene pankayankhula zodzitama.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinali kulingirira za nyangazi, taonani, pakati pa izo panaphuka nyanga yina, ndiyo yaing'ono; patsogolo pace zitatu za nyanga zoyambazi zinazulidwa ndi mizu yomwe; ndipo taonani, m'nyanga m'menemo munali maso ngati maso a munthu, ndi pakamwa palikunena zazikuru.