Daniel 7:9 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zovala zake zinali za mbu ngati chipale chofewa, ndi tsitsi la pa mutu pake ngati ubweya woyera, mpando wachifumu unali malawi amoto, ndi njinga zake moto woyaka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine ndikuyangʼanabe ndinaona “mipando yaufumu ikukhazikitsidwa, ndipo Mkulu Wachikhalire anakhala pa mpando wake. Zovala zake zinali zoyera ngati chisanu chowundana; tsitsi la kumutu kwake linali loyera ngati thonje. Mpando wake waufumu unali wonga malawi a moto, ndipo mikombero yake yonse inkayaka moto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yacifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zobvala zace zinali za mbu ngati cipale cofewa, ndi tsitsi la pa mutu pace ngati ubweya woyera, mpando wacifumu unali malawi amoto, ndi njinga zace moto woyaka.