Daniel 8:11 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inde inadzikulitsa kufikira kwa kalonga wa khamulo, nimchotsera nsembe yopsereza yachikhalire, ndi pokhala malo ake opatulika panagwetsedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inadzikuza yokha mpaka kufikira kwa mfumu ya gululo: inathetsa nsembe zimene zinkaperekedwa tsiku ndi tsiku, ndipo inagwetsa nyumba yake yopatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inde inadzikulitsa kufikira kwa kalonga wa khamulo, nimcotsera nsembe yopsereza yacikhalire; ndi pokhala malo ace opatulika panagwetsedwa.