Daniel 8:19 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Taona, ndidzakudziwitsa chimene chidzachitika pa chitsiriziro cha mkwiyowo; pakuti pa nthawi yoikika mpakutha pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati, “Ine ndikuwuza zimene zidzachitike ukadzatha mkwiyo, chifukwa masomphenyawa ndi a nthawi ya chimaliziro.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Taona, ndidzakudziwitsa cimene cidzacitika pa citsiriziro ca mkwiyowo; pakuti pa nthawi yoikika mpakutha pace,