Daniel 8:25 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mwa kuchenjera kwake adzapindulitsa chinyengo m'dzanja mwake, nadzadzikuza m'mtima mwake; ndipo posatekeseka anthu, adzaononga ambiri; adzaukiranso kalonga wa akalonga, koma adzathyoledwa popanda dzanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha kuchenjera kwake chinyengo chidzachuluka pa nthawi ya ulamuliro wake, ndipo idzadzikuza kuposa onse. Pamene oyera mtima adzaona ngati kuti ali otetezedwa, iyo idzawononga ambiri ndi kuwukira ngakhale Mfumu ya mafumu. Komabe idzawonongedwa, koma osati ndi mphamvu za munthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mwa kucenjera kwace adzapindulitsa cinyengo m'dzanja mwace, nadzadzikuza m'mtima mwace; ndipo posatekeseka anthu, adzaononga ambiri; adzaukiranso kalonga wa akalonga, koma adzatyoledwa popanda dzanja.