Daniel 9:12 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anakwaniritsa mau ake adanenawo, kutitsutsa ife ndi oweruza athu otiweruza, ndi kutitengera choipa chachikulu; pakuti pansi pa thambo lonse sipanachitika monga umo panachitikira Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mwakwaniritsa mawu amene munayankhula otitsutsa ife ndi otsutsa otilamulira potibweretsera tsoka lalikulu. Pa dziko lapansi sipanachitikenso zinthu ngati zimene zaonekera Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anakwaniritsa mau ace adanenawo, kutitsutsa ife ndi oweruza athu otiweruza, ndi kutitengera coipa cacikuru; pakuti pansi pa thambo lonse sipanacitika monga umo panacitikira Yerusalemu.