Daniel 9:14 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Yehova wakhala maso pa choipacho, ndi kutifikitsira icho; pakuti Yehova Mulungu wathu ali wolungama mu ntchito zake zonse azichita; ndipo sitinamvera mau ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehova anakonza kuti atigwetsere tsoka limeneli, ndipo wachitadi popeza Yehova Mulungu wathu ndi wolungama mu chilichonse amachita; chikhalirecho ife sitinamumvere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Yehova wakhala maso pa coipaco, ndi kutifikitsira ico; pakuti Yehova Mulungu wathu ali wolungama mu nchito zace zonse azicita; ndipo sitinamvera mau ace.