Daniel 9:16 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ambuye, monga mwa chilungamo chanu chonse, mkwiyo wanu ndi ukali wanu zitembenuketu, zichoke kumudzi wanu Yerusalemu, phiri lanu lopatulika; pakuti mwa zochimwa zathu, ndi mphulupulu za makolo athu, Yerusalemu ndi anthu anu asanduka chotonza cha onse otizungulira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Ambuye, molingana ndi zochita zanu zolungama, tikukupemphani kuti muchotse mkwiyo ndi ukali wanu pa Yerusalemu mzinda wanu, phiri lanu loyera. Machimo athu ndi mphulupulu za makolo athu zachititsa kuti onse otizungulira atonze Yerusalemu ndi anthu anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ambuye, monga mwa cilungamo canu conse, mkwiyo wanu ndi ukali wanu zitembenuketu, zicoke ku mudzi wanu Yerusalemu, phiri lanu lopatulika; pakuti mwa zocimwa zathu, ndi mphulupulu za makolo athu, Yerusalemu ndi anthu anu asanduka cotonza ca onse otizungulira.