Daniel 9:18 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu wanga, tcherani khutu, nimumvere, tsegulani maso anu, nimupenye zopasuka zathu, ndi mudzi udatchedwawo dzina lanu; pakuti dzina lanu; pakuti sititula mapembedzero athu pamaso panu, chifukwa cha ntchito zathu zolungama, koma chifukwa cha zifundo zanu zochuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tcherani khutu, Inu Mulungu, ndipo imvani; tsekulani maso anu ndipo onani mabwinja athu ndi mzinda umene umadziwika ndi dzina lanu. Sitikupempha chifukwa chakuti ndife olungama, koma chifukwa cha kukula kwa chifundo chanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu wanga, cherani khutu, nimumvere, tsegulani maso anu, nimupenye zopasuka zathu, ndi mudzi udachedwawo dzina lanu; pakuti sititula mapembedzero athu pamaso panu, cifukwa ca nchito zathu zolungama, koma cifukwa ca zifundo zanu zocuruka.