Daniel 9:19 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ambuye, imvani; Ambuye khululukirani; Ambuye, mverani nimuchite; musachedwa, chifukwa cha inu nokha, Mulungu wanga; pakuti mudzi wanu ndi anthu anu anatchedwa dzina lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Ambuye imvani mawu athu! Ambuye khululukani! Ambuye timvereni, ndipo muchitepo kanthu! Kuti anthu adziwe kuti Inu ndinu Mulungu wanga musachedwe chifukwa mzinda wanu ndi anthu anu amadziwika ndi dzina lanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ambu ye, imvani; Ambuye, khululukirani; Ambuye, mverani nimucite; musacedwa, cifukwa ca inu nokha, Mulungu wanga; pakuti mudzi wanu ndi anthu anu anachedwa dzina lanu.