Daniel 9:21 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
inde pakunena ine m'kupemphera, munthu uja Gabriele, amene ndidamuona m'masomphenya poyamba paja, anauluka mwaliwiro nandikhudza ngati nthawi yakupereka nsembe ya madzulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gabrieli, munthu uja amene ndinamuona mʼmasomphenya poyambirira, anabwera kwa ine mowuluka. Iyi inali nthawi ya nsembe ya madzulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
inde pakunena ine m'kupemphera, munthu uja Gabrieli, amene ndidamuona m'masomphenya poyamba paja, anauluka mwaliwiro nandikhudza ngati nthawi yakupereka nsembe ya madzulo.