Daniel 9:24 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masabata makumi asanu ndi awiri alamulidwira anthu a mtundu wako ndi mudzi wako wopatulika, kumaliza cholakwacho, ndi kutsiriza machimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa chilungamo chosalekeza, ndi kukhomera chizindikiro masomphenya ndi zonenera, ndi kudzoza malo opatulika kwambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Zaka 490 zinayikidwa kuti anthu a mtundu wako ndi mzinda wanu woyera aleke zoyipa, asiye tchimo. Iwo adzapereka dipo kupepesera zolakwa zawo. Zikadzatero anthu adzaonetsa moyo wachilungamo nthawi zonse. Izi zidzatsimikiza zimene unaziona mʼmasomphenya zija ndi zimene ananenera aneneri. Malo opatulika adzakhazikitsidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masabata makumi asanu ndi awiri alamulidwira anthu amtundu wako ndi mudzi wako wopatulika, kumariza colakwaco, ndi kutsiriza macimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa cilungamo cosalekeza, ndi kukhomera cizindikilo masomphenya ndi zonenera, ndi kudzoza malo opatulikitsa.