Daniel 9:26 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mudzi ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patatha zaka 434, Wodzozedwayo adzaphedwa ndipo sadzakhala ndi aliyense. Anthu a wolamulira amene adzabwere adzawononga mzinda ndi Nyumba ya Mulungu. Kutha kwake kudzafika ngati chigumula. Komabe nkhondo idzapitirira mpaka chiwonongeko chimene Mulungu ananeneratu chitachitika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mudzi ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwace kudzakhala kwa cigumula, ndi kufikira cimariziro kudzakhala nkhondo; cipasuko calembedweratu.