Daniel 9:4 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza, ndi kuti, Ambuye Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakuwasungira pangano ndi chifundo iwo akukukondani, ndi kusunga malamulo anu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza kuti tinachimwa: Ndinati, “Inu Ambuye, Mulungu wamkulu ndi woopsa, amene mumasunga pangano lanu la chikondi kwa onse amene amakukondani ndi kumvera malamulo anu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kubvomereza, ndi kuti, Ambuye Mulungu wamkuru ndi woopsa, wakuwasungira pangano ndi cifundo iwo akukukondani, ndi kusunga malamulo anu,