Daniel 9:7 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ambuye, chilungamo ncha Inu, koma kwa ife manyazi a nkhope yathu, monga lero lino; kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, ndi kwa Aisraele onse okhala pafupi ndi okhala kutali, kumaiko onse kumene mudawaingira, chifukwa cha kulakwa kwao anakulakwirani nako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ambuye ndinu olungama, koma lero tili ndi manyazi, ife anthu a ku Yuda, a ku Yerusalemu ndi Israeli yense, apafupi ndi akutali omwe, ku mayiko onse kumene munatipirikitsira chifukwa cha kusakhulupirika kwathu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ambuye, cilungamo nca Inu, koma kwa ife manyazi a nkhope yathu, monga lero lino; kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, ndi kwa Aisrayeli onse okhala pafupi ndi okhala kutali, ku maiko onse kumene mudawaingira, cifukwa ca kulakwa kwao anakulakwirani nako.