Deuteronomy 1:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero ndidasankha atsogoleri anu, anthu anzeru ndi odziŵa zinthu bwino, ndipo ndidaŵaika kuti aziyang'anira ena magulu a anthu zikwi zingapo, ena a anthu mazana angapo, ena a anthu makumi asanu, ndipo enanso a anthu khumi. Enanso ndidaŵasankha kuti akhale nduna pakati pa mafuko anuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero ndinatenga akulu a mafuko anu, amuna anzeru, ndi odziwika, ndi kuwaika akhale akulu anu, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndi atsogoleri a makumi, ndi akapitao, a mafuko anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ndinatenga anthu otsogolera mafuko anu, anzeru ndi omwe mumawalemekeza, ndipo ndinawayika kuti azikulamulirani mʼmagulu a 1,000, ena 100, ena makumi asanu ndi ena khumi, kuti akhalenso ngati akapitawo a mafuko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero ndinatenga akuru a mapfuko anu, amuna anzeru, ndi odziwika, ndi kuwaika akhale akuru anu, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndi atsogoleri a makumi asanu, ndi atsogoleri a makumi, ndi akapitao, a mapfuko anu.