Deuteronomy 1:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi imene ija, ndidaŵalangiza aweruzi anuwo kuti, “Mumve milandu imene ili pakati pa anthu anu. Mlandu uliwonse muuweruze bwino, kaya ndi wa anthu a mtundu wanu, kapena wa alendo amene amakhala nao pakati panu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinauza oweruza anu muja, ndi kuti, Mverani milandu ya pakati pa abale anu, ndi kuweruza kolungama pakati pa munthu ndi mbale wake, ndi mlendo wokhala naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo pa nthawi imeneyo ndinawawuza olamula anu kuti, “Muzimva milandu ya pakati pa abale anu ndi kuweruza mosakondera, kaya mlanduwo uli pakati pa Aisraeli okhaokha kapena mmodzi wa iwo ndi mlendo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinauza oweruza anu muja, ndi kuti, Mverani milandu ya pakati pa abale anu, ndi kuweruza kolungama pakati pa munthu ndi mbale wace, ndi mlendo wokhala naye.