Deuteronomy 1:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musamakondere poweruza. Aliyense, munthu wamba kapena wamkulu, mumuweruze chimodzimodzi. Musamaopa wina aliyense, chifukwa chiweruzo chonse ndi cha Mulungu. Mlandu wina ukakulakani, mubwere nawo kwa ine, ndipo ndidzaugamula ndine.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamasamalira munthu poweruza mlandu; ang'ono ndi akulu muwamvere chimodzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza chiweruzo ncha Mulungu; ndipo mlandu ukakukanikani mubwere nao kwa ine, ndidzaumva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Osamayangʼana nkhope poweruza koma muzimvetsera aangʼono ndi aakulu omwe chimodzimodzi. Musamaope munthu aliyense, pakuti chiweruzo ndi cha Mulungu. Muzindibweretsera mlandu uliwonse wovuta ndipo ndidzaumva.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamasamalira munthu poweruza mlandu; ang'ono ndi akuru muwamvere m'modzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza ciweruzo nca Mulungu; ndipo mlandu ukakulakani mubwere nao kwa ine, ndidzaumva.