Deuteronomy 1:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ife tidachita zimene Chauta, Mulungu wathu, adatilamula. Tidachoka ku phiri la Horebu ndipo tidabzola chipululu chachikulu ndi choopsa chija chimene mudachiwona pa njira yopita ku dziko lamapiri la Aamori. Titafika ku Kadesi-Baranea,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo tinayenda ulendo kuchokera ku Horebu, ndi kubzola m'chipululu chachikulu ndi choopsa chija chonse munachionachi, pa njira ya ku mapiri a Aamori, monga Yehova Mulungu wathu anatiuza; ndipo tinadza ku Kadesi-Baranea.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono monga Yehova Mulungu wathu anatilamulira, tinanyamuka kuchoka ku Horebu ndi kupita cha ku dziko lamapiri la Aamori kudzera ku chipululu chachikulu ndi choopsa chija munachionachi, kotero kuti tinakafika ku Kadesi Barinea.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo tinayenda ulendo kucokera ku Horebe, ndi kubzyola m'cipululu cacikuru ndi coopsa ciija conse munacionaci, pa njira ya ku mapiri a Aamori, monga Yehova Mulungu wathu anatiuza; ndipo tinadza ku Kadesi Barinea.