Deuteronomy 1:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi limenelitu dziko lomwe Chauta, Mulungu wa makolo anu, akukupatsani. Pitani, kakhaleni m'menemo monga momwe adakulamulirani. Musaope kapena kuchita mantha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, Yehova Mulungu wanu wapatsa dzikoli pamaso panu; kwerakoni, landirani, monga Yehova Mulungu wa makolo anu, wanena ndi inu; musamachita mantha, musamatenga nkhawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dzikoli. Pitani ndi kulitenga monga Yehova, Mulungu wa makolo anu anakuwuzirani. Musaope kapenanso kugwa mphwayi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, Yehova Mulungu wanu wapatsa dzikoli pamaso panu; kwerakoni, landirani, monga Yehova Mulungu wa makolo anu, wanena ndi inu; musamacita mantha, musamatenga nkhawa.