Deuteronomy 1:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma paja inu mudabwera kwa ine nkumanena kuti, “Tiyeni titume anthu akaliwone dzikolo, kuti adzatiwuze njira yabwino yoti tidzadzere, ndipo adzatifotokozere za m'mene iliri mizinda yakumeneko.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munayandikiza kwa ine inu nonse, ndi kuti, Titumize amuna atitsogolere, kuti akatizondere dziko ndi kutibwezera mau akunena za njira ya kukwera nayo ife pomka komwemo, ndi za midzi yoti tidzafikako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono nonse munabwera kwa ine ndi kuti, “Tiyeni titumize anthu ayambe apita kuti akazonde dzikolo ndi kutibweretsera mawu pa za njira yomwe tidzere ndi za mizinda imene tikafikireko.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munayandikiza kwa ine inu nonse, ndi kuti, Titumize amuna atitsogolere, kuti akatizondere dziko ndi kutibwezera mau akunena za njira ya kukwera nayo ife pomka komweko, ndi za midzi yoti tidzafikako.