Deuteronomy 1:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi tikapeza dziko lanji kumeneko? Abale athu aja atidederetsa potiwuza kuti anthu akumeneko ngamphamvu ndi aatali kupambana ife. Akutinso mizindayo njaikulu, ya malinga ofika mpaka m'mwamba. Ndiponso akuti kumeneko adaona ziphona, zidzukulu za Aanaki.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tikwere kuti? Abale athu atimyukitsa mitima yathu, ndi kuti, Anthuwo ndiwo akulu ndi atali akuposa ife; midzi ndi yaikulu ndi ya malinga ofikira m'mwamba: tinaonakonso ana a Anaki.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tigwire mtengo wanji? Abale athu anatitayitsa mtima. Iwo akuti, ‘Anthuwo ndi amphamvu ndi aatali kuposa ife, mizindayo ndi yayikulu ndipo mipanda yake ndi yayitali yofika kumwamba. Ife tinaonanso Aanaki kumeneko.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tikwere kuti? abale athu atimyukitsa mitima yathu, ndi kuti, Anthuwo ndiwo akulu ndi atali akuposa ife; midzi ndi yaikulu ndi ya malinga ofikira m'mwamba: tinaonakonso ana a Anaki.