Deuteronomy 1:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku loyamba la mwezi wa 11, pa chaka cha 40 kuyambira pamene adatuluka m'dziko la Ejipito, Mose adauza anthu a ku Israele zonse zimene Chauta adamlamula kuti anene kwa anthuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, chaka cha makumi anai, mwezi wakhumi ndi umodzi, tsiku loyamba la mweziwo, Mose ananena ndi ana a Israele, monga mwa zonse Yehova adamlamulira awauze;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka cha makumi anayi, pa tsiku loyamba la mwezi 11, Mose anafotokozera Aisraeli zonse zimene Yehova anamulamula zokhudza iwowo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, caka ca makumi anai, mwezi wakhumi ndi umodzi, tsiku loyamba la mweziwo, Mose ananena ndi ana a Israyeli, monga mwa zonse Yehova adamlamulira awauze;