Deuteronomy 1:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Kalebe yekha, mwana wa Yefune, ndiye amene adzaloŵe. Iyeyo adakhala ndithu wokhulupirika kwa Ine, choncho dziko adalipenyalo ndidzalipatsadi kwa iye ndi kwa zidzukulu zake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Kalebe mwana wa Yefune, iye adzaliona; ndidzampatsa iye dziko limene anapondapo, ndi ana ake; popeza analimbika ndi kutsata Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kupatula Kalebe mwana wa Yefune. Iye adzaliona, ndipo ndidzamupatsa iye ndi adzukulu ake, dziko limene adzapondamo popeza anatsata Yehova ndi mtima wake wonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Kalebi mwana wa Yefune, iye adzaliona; ndidzampatsa iye dziko limene anapondapo, ndi ana ace; popeza analimbika ndi kutsata Yehova.