Deuteronomy 1:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adatiwuza tonsefe kuti, “Makanda anu amene mudati adzagwidwa ndi adani, ndiponso ana anu amene akadali aang'ono, amene sadziŵa chabwino kapena choipa pa lero lino, ndiwo adzaloŵe m'dzikolo. Ndidzalipatsa kwa iwowo ndipo adzakhalamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana anu amene mudanena, Adzakhala ogulidwa, ndi ana anu osadziwa chabwino kapena choipa ndi pano, iwo adzalowamo, ndidzawapatsa iwo ili, adzalilandira ndi iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo angʼonoangʼono amene munati adzagwidwa ukapolo, ana anu amene sanadziwe kusiyanitsa chabwino ndi choyipa, amenewo adzalowa mʼdzikolo. Ndidzalipereka kwa iwo ndipo lidzakhala lawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana anu amene mudanena, Adzakhala ogulidwa, ndi ana anu osadziwa cabwino kapena coipa ndi pano, iwo adzalowamo, ndidzawapatsa iwo ili, adzalilandira ndi iwo.