Deuteronomy 1:41 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mudayankha kuti, “Ife tachimwira Chauta. Koma tsopano tidzamenya nkhondo monga momwe Chauta wathu adatilamulira.” Pamenepo aliyense mwa inu adatenga zida zake zankhondo, namaganiza kuti nkwapafupi kugonjetsa dziko lamapirilo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo munayankha ndi kunena ndi ine, Tachimwira Yehova, tidzakwera ndi kuthira nkhondo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu atiuza. Ndipo munadzimangira munthu yense zida zake za nkhondo, nimunakonzeka kukwera kunka kumapiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo inuyo munati, “Tachimwa pamaso pa Yehova. Tipita ndi kukachita nkhondo monga Yehova Mulungu wathu watilamulira.” Choncho aliyense wa inu anavala zankhondo, ndi kuganiza kuti nʼkosavuta kupita mʼdziko la mapiri lija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo munayankha ndi kunena ndi ine, Tacimwira Yehova, tidzakwera ndi kuthira mkhondo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu atiuza. Ndipo munadzimangira munthu yense zida zace za nkhondo, nimunakonzeka kukwera kumka kumapiri.