Deuteronomy 1:42 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta adandiwuza kuti, “Uŵachenjeze kuti asaŵapute Aamoriwo, chifukwa Ine sindidzakhala nawo, ndipo adani aowo adzaŵagonjetsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehova anati kwa ine, Nena nao, Musakwerako, kapena kuthira nkhondo; popeza sindili pakati panu; angakukantheni adani anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova anandiwuza kuti, “Awuze anthuwa kuti, ‘Musapite kukachita nkhondo chifukwa Ine sindidzakhala nanu. Mudzagonjetsedwa ndi adani anu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yehova anati kwa ine, Nena nao, Musakwerako, kapena kuthira nkhondo; popeza sindiri pakati panu; angakukantheni adani anu.