Deuteronomy 1:44 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Aamori okhala m'mapiriwo adakutulukirani nakuthamangitsani ngati njuchi, ndipo adakukanthani kuchokera ku Seiri mpaka ku Horoma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Aamori, akukhala m'mapiri muja, anatuluka kukomana ndi inu, nakupirikitsani, monga zimachita njuchi, nakukanthani m'Seiri, kufikira ku Horoma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aamori amene ankakhala mʼmapiriwo anatuluka kukakumana nanu ndipo anakuthamangitsani ngati gulu la njuchi ndipo anakukanthani kuchokera ku Seiri, njira yonse mpaka ku Horima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Aamori, akukhala m'mapiri muja, anaturuka kukomana ndi inu, nakupitikitsani, monga zimacita njuci, nakukanthani m'Seiri, kufikira ku Horima.