Deuteronomy 1:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyamukani muyambepo kuyenda. Pitani ku dziko lamapiri la Aamori, ndi konse kumene kumakhala anzao a Aamoriwo ku chigwa cha Araba, ku dziko lamapiri ndi ku zigwa, ku Negebu ndi pamphepete pa Nyanja yaikulu, ku dziko la Akanani ndi ku Lebanoni, mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
bwererani, yendani ulendo wanu ndi kumuka ku mapiri a Aamori, ndi koyandikizana nao, kuchidikha, kumapiri, ndi kunsi ndi kumwera, ndi kumphepete kwa nyanja, dziko la Akanani, ndi Lebanoni, kufikira mtsinje waukulu wa Yufurate.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sasulani msasa ndipo pitani ku dziko la mapiri la Aamori. Pitani kwa anthu onse oyandikana nawo ku Araba, ku mapiri, mʼmbali mwa mapiri a ku madzulo, ku Negevi ndiponso mʼmbali mwa nyanja, ku dziko la Akanaani ndi ku Lebanoni mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
bwererani, yendani ulendo wanu ndi kumuka ku mapiri a Aamori, ndi koyandikizana nao, kucidikha, kumapiri, ndi kunsi ndi kumwela, ndi kumphepete kwa nyanja, dziko la Akanani, ndi Lebano, kufikira nyanja yaikuru Firate.