Deuteronomy 10:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
(Aisraele adachoka ku Beeroti-Bene-Yaakani, napita ku Mosera. Aroni atamwalira adaikidwa komweko. Mwana wake Eleazara ndiye amene adaloŵa m'malo mwake, kukhala wansembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Israele anayenda ulendo wao kuchokera ku zitsime za ana a Yaakani kufikira ku Mosera. Kumeneko anamwalira Aroni, ndi kumeneko anamuika; ndipo Eleazara mwana wake anachita ntchito ya nsembe m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli anayenda kuchokera ku Beeroti Beni Yaakani mpaka ku Mosera. Kumeneko Aaroni anamwalira nayikidwa mʼmanda, ndipo mwana wake Eliezara anakhala wansembe mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Israyeli anayenda ulendo wao kucokera ku zitsime za ana a Yaakani kufikira ku Mosera. Kumeneko anamwalira Aroni, ndi kumeneko anamuika; ndipo Eleazara mwana wace anacita nchito ya nsembe m'malo mwace.