Deuteronomy 10:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo Chauta adasankha a fuko la Levi, kuti azinyamula Bokosi lachipangano, azikhala pamaso pa Chauta ndi kumatumikira, ndiponso kuti azidalitsa anthu m'dzina la Chauta. Ndiwo amene amachita zimenezi mpaka lero lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku aja Yehova anapatula fuko la Levi, linyamule likasa la chipangano la Yehova, liimirire pamaso pa Yehova kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lake kufikira lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi imeneyo Yehova anapatula fuko la Levi kuti anyamule bokosi la pangano la Yehova lija, kuti ayimirire pamaso pa Yehova, kutumikira ndi kunena madalitso pa dzina lake monga amachitira mpaka lero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku aja Yehova anapatula pfuko la Levi, linyamule likasa la cipangano la Yehova, liimirire pamaso pa Yehova kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lace kufikira lero lino.