Deuteronomy 11:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko limene mukukakhalamolo likusiyana ndi dziko la Ejipito kumene mudachokera. Kumene kuja munkati mukafesa mbeu zanu, munkachita kuthirira ngati m'madimba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti dziko limene mumkako kulilandira ndi losanga dziko la Ejipito lija mudatulukako, kumene kuja munafesa mbeu zanu, ndi kuzithirira ndi phazi lanu, monga munda watherere;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko limene mukukalanda ndi kulowamo silokhala ngati dziko la ku Igupto kumene mukuchokera ayi, kuja mumadzala mbewu ndi kumathirira ndi mapazi anu ngati ku dimba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti dziko limene mumkako kulilandira ndi losanga dziko la Aigupto lija mudaturukako, kumene kuja munafesa mbeu zanu, ndi kuzithirira ndi phazi lanu, monga munda watherere;