Deuteronomy 11:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
chifukwa Chauta adzakukwiyirani, adzakumanani mvula, ndipo nthaka sidzabalanso zipatso zake. Motero mudzaonongeka msanga m'dziko lokomali limene Chauta akukupatsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kuti Mulungu angapse mtima pa inu, nangatseke kumwamba, kuti isowe mvula, ndi kuti nthaka isapereke zipatso zake; ndi kuti mungaonongeke msanga m'dziko lokomali Yehova akupatsani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukatero Yehova Mulungu wanu adzakukwiyirani kwambiri, nadzaletsa thambo kuti lisabweretsenso mvula ndipo dziko silidzapereka zokolola. Choncho mudzawonongeka msanga mʼdziko limene Yehova akukupatsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kuti Mulungu angapse mtima pa inu, a nangatseke kumwamba, kuti isowe mvula, ndi kuti nthaka isapereke zipatso zace; ndi kuti mungaonongeke msanga m'dziko lokomali Yehova akupatsani.