Deuteronomy 11:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Popeza kuti si ana anu, koma ndinu amene mudazidziŵa ndi kuziwona zakale zonsezo, mukumbukire za Chauta, Mulungu wanu. Ukulu wake mudauwona, mudaonanso dzanja lake lamphamvu ndi mkono wake wotambalitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo dziwani lero lino; pakuti sindinena ndi ana anu osadziwa, ndi osapenya kulanga kwa Yehova Mulungu wanu, ukulu wake, dzanja lake lamphamvu, ndi mkono wake wotambasuka,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lero kumbukirani kuti si ana anu amene anaona ndi kulawa chilango cha Yehova Mulungu wanu: ukulu wake, dzanja lake lamphamvu, mkono wake wotambasuka;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo dziwani lero lino; pakuti sindinena ndi ana anu osadziwa, ndi osapenya kulanga kwa Yehova Mulungu wanu, ukulu wace, dzanja lace lamphamvu, ndi mkono wace wotambasuka,