Deuteronomy 11:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muzimvera mokhulupirika zonse zimene ndakuuzanizi. Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, muzichita zonse zimene akulamulani, ndipo mukhale okhulupirika kwa Iye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mukasunga chisungire malamulo awa onse amene ndikuuzani kuwachita; kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake zonse, ndi kummamatira;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukatsatira mosamalitsa malamulo amene ndikukupatsaniwa, kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda mʼnjira zake zonse ndi kumugwiritsitsa Iye
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mukasunga cisungire malamulo awa onse amene ndikuuzani kuwacita; kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zace zonse, ndi kummamatira;