Deuteronomy 11:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene adzakuletseni. Kulikonse kumene mudzapite m'dziko limenelo, anthu azidzakuwopani, monga momwe Mulungu wakulonjezerani kuti adzaŵachititsa mantha anthu amenewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Palibe munthu adzaima pamaso panu; Yehova Mulungu wanu adzanjenjemeretsa ndi kuopsa dziko lonse mudzapondapo, chifukwa cha inu, monga anenana ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palibe munthu amene adzalimbana nanu. Monga analonjezera, Yehova adzachititsa kuti anthu onse mʼdziko limene mukupitalo adzachite nanu mantha ndi kukuopani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Palibe munthu adzaima paraaso panu; Yehova Mulungu wanu adzanjenjemeretsa ndi kuopsa dziko lonse mudzapondapo, cifukwa ca inu, monga ananena ndi inu.