Deuteronomy 11:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akadzakuloŵetsani m'dziko limene mukupita kukakhalamolo, muzikalalika madalitso ameneŵa mutakwera pa phiri la Gerizimu, koma matembereroŵa muzikaŵalalika mutakwera pa phiri la Ebala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzakhala, atakulowetsani Yehova Mulungu wanu m'dziko limene mumkako kulilandira, munene mdalitso pa phiri la Gerizimu, ndi temberero pa phiri la Ebala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Mulungu wanu akakakufikitsani mʼdziko mukukalandalo kuti mulowemo mukanene za madalitso pa Phiri la Gerizimu, ndi za matemberero pa Phiri la Ebala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzakhala, atakulowetsani Yehova Mulungu wanu m'dziko limene mumkako kulilandira, munene mdalitso pa phiri la Gerizimu, ndi temberero pa phiri la Ebala.