Deuteronomy 11:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mapiri aŵiri ameneŵa ali chakuzambwe kutsidya kwa mtsinje wa Yordani, m'dziko la Akanani amene amakhala m'chigwa cha Yordani, pafupi ndi mitengo ya thundu ya ku More, kuyang'anana ndi Giligala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sakhala kodi tsidya lija la Yordani, m'tseri mwake mwa njira yake yolowa dzuwa, m'dziko la Akanani, akukhala m'chidikha, pandunji pake pa Giligala, pafupi pa mathundu a More?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga mudziwa, mapiriwa ali kutsidya kwa Yorodani, kumadzulo kolowera dzuwa, kufupi ndi mitengo ya thundu ya More, mʼdziko la Akanaani aja okhala ku Araba moyangʼanana ndi Giligala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sakhala kodi tsidya lija la Yordano, m'tseri mwace mwa njira yace yolowa dzuwa, m'dziko la Akanani, akukhala m'cidikha, pandunji pace pa Giligala, pafupi pa mathunda a More?