Deuteronomy 11:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudaona zimene adachita polimbana ndi ankhondo a ku Ejipito ndiponso ndi akavalo ndi magaleta ao. Pamene iwo ankathamangitsa inu, mudaona m'mene Chauta adalamulira madzi a Nyanja Yofiira kuti aŵaphimbe ndi kuŵaononga onsewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi chochitira Iye nkhondo ya Ejipito, akavalo ao, ndi agaleta ao; kuti anawamiza m'madzi a Nyanja Yofiira, muja anakutsatani m'mbuyo, ndi kuti Yehova anawaononga kufikira lero lino;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
zimene Iye anachita kwa gulu lankhondo la Aigupto, kwa akavalo ndi magaleta awo, mmene Iye anawamizira ndi madzi a mu Nyanja Yofiira pamene amakuthamangitsani, ndi mmene Yehova anawagonjetsera kufikira lero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi cocitira iye nkhondo ya Aigupto, akavalo ao, ndi agareta ao; kuti anawamiza m'madzi a Nyanja Yofiira, muja anakutsatani m'mbuyo, ndi kuti Yehova anawaononga kufikira lero lino;