Deuteronomy 11:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudaona zimene Chauta adachita pa Datani ndi pa Abiramu, ana a Eliyabu, a fuko la Rubeni. Pamaso pa Aisraele onse nthaka idatsekuka nkuŵakwirira anthuwo, pamodzi ndi a m'banja mwao, mahema ao ndi zoŵeta zao zomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi chimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, mwana wa Rubeni; muja nthaka inatsegula pakamwa pake, ndi kuwameza iwo, ndi mabanja ao, ndi mahema ao, ndi za moyo zonse zakuwatsata pakati pa Israele wonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndi zimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana aamuna a Eliabu mwana wa Rubeni, pamene nthaka inatsekula pakamwa pake pakati pa Aisraeli onse ndi kuwameza pamodzi ndi katundu wawo, matenti awo ndi chilichonse chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi cimene anacitira Datani ndi Abiramu, ana a Eliabu, mwana wa Rubeni; muja nthaka inatsegula pakamwa pace, ndi kuwameza iwo, ndi mabanja ao, ndi mahema ao, ndi za moyo zonse zakuwatsata pakati pa Israyeli wonse.