Deuteronomy 12:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Naŵa malamulo ndi malangizo onse amene mudzayenera kuŵamvera nthaŵi zonse mudzakhale m'dziko limene Chauta, Mulungu wa makolo anu, akukupatsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Awa ndi malemba ndi maweruzo, muziwasamalirawa kuwachita m'dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu anakupatsani likhale lanulanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu pa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Awa ndi malangizo ndi malamulo amene muyenera kusamalitsanso kuti muwatsatire mʼdziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu wakupatsani kuti mutenge pa nthawi yonse imene muti mudzakhale mʼdzikomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Awa ndi malemba ndi maweruzo, muziwasamalirawa kuwacita m'dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu anakupatsani likhale lanu lanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu pa dziko lapansi.