Deuteronomy 12:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukaoloka mtsinje wa Yordani, Chauta, Mulungu wanu, adzakulolani kukakhala m'dziko limene Chauta adzakupatsani ngati choloŵa chanu. Adzakutchinjirizani kwa adani anu onse, kuti mukhale mwamtendere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mudzaoloka Yordani, ndi kukhala m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akulandiritsani; ndipo adzakupumulitsani akulekeni adani anu onse pozungulirapo, ndipo mudzakhala mokhazikika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mudzawoloka Yorodani ndi kukhazikika mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, ndipo Iye adzakupatsani inu mpumulo ku adani anu okuzungulirani kuti mukhale motchinjirizidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mudzaoloka Yordano, ndi kukhala m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akulandiritsani; ndipo adzakupumulitsani akulekeni adani anu onse pozungulirapo, ndipo mudzakhala mokhazikika.