Deuteronomy 12:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Chauta adzasankhula malo oti anthu azidzapembedzerako, ndipo inu muzidzabwera kumeneko ndi zonse zimene ndakulamulanizi, monga nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zanu zinanso, zopereka zanu zachikhumi ndi zopereka zanu zina, ndiponso mphatso zanu zapadera zimene mumalonjeza kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuti azikhalako muzikabweretsako chilichonse chimene ndikulamulirani inu: zopereka ndi nsembe zanu zopsereza, chakhumi chanu ndi mphatso zapadera, ndi chuma chanu chonse chosankhika chimene munalonjeza kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lace, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.